Gulu la amayi lolimbikitsa bata ndi mtendere la Kanyenda Women’s Forum m'boma la Nkhotakota lati lipitiriza kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pofalitsa uthenga wake pamene dziko lino layandikira tsiku la chisankho.
Wapampando wa gululi, Alinafe Major Kamunthu ndiye wanena izi pamapeto a ulendo wandawala omwe gululi linakoza lachinayi pa msika wa Dwangwa m’boma la Nkhotakota ndi cholinga cholimbikitsa mzika maka achinyamata kuti apewe andale kuti awagwiritse ntchito poyambitsa ziwawa ndi kunyoza ena pa nthawi ya misonkhano yokopa anthu.
“tikufuna anthu onse akhale otetezeka chifukwa nthawi yokopa anthu ino kumakhala ziwawa ndi zipolowe zochuluka zodza Kamba kosiyana maganizo pandale zomwe zimadzetsa kuvulala komanso kutaya miyoyo kwa anthu kumene,” anatero Major.
Iye anaonjezera kuti ndikofunikaso kuti amayi omwe akuyimira m’maudindo osiyanasiyana apatsiwe chilimbikitso powavotera m’maudindo posatengera chipani chomwe akuyimira, potsindika kuti ali ndi kuthekera kolamulira, ndikupanga ziganizo zopititsa patsogolo chitukuko kudera ngakhaleso m’dziko.
Lawrence Wasili, wapampando wa Nkhunga Youth Friendly Health Services wavomereza kuti achinyamata ambiri amagwiritsidwa ntchito ndi andale ndipo zimakhala zovetsa chisoni kuti achinyamatawa akagwa m’mavuto amasiyidwa opanda thandizo lililonse.
“Tipitiriza kumema achinyamata anzathu kuti asamalore andale omwe akuwatuma kumakachita zinthu zoipa ndicholinga choti achinyamatawa tikhale otetezeka komaso kuti kumadera omwe tikuchokera kukhale kwa bata ndi mtendere,” anatero Wilisi.
Mmawu ake, mkulu oyenetsa nchito za Women Voice for Peace ku bungwe la Umunthu Plus, Matias Nkhoma wati amayi ndi achinyamata ndiwo amavutika kudera kukachitika ziwawa ndi zopolowe, kotero ndikofunika kulimbikitsa uthenga wa bata ndi mtendere pakati pawo kuti azipewa zinthu zisadafike povuta.
“Udindo olimbikitsa bata ndi mtendere kudera uli m’manja mwa aliyense posatengera chipembedzo, chipani kapena kochokera, choncho tipitiriza kupereka upangiri polimbikitsa bata ndi mtendere komaso kuti amayi azikhala nawo m’maudindo autsogoleri,” watero Nkhoma.
Bungwe la umunthu plus likugwira ntchito yolimbikitsa bata ndi mtendere m’boma la Nkhotakota pansi pa polojekiti ya Women Voice for Peace ndi thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la Women Peace & Humanitarian Fund kudzera ku bungwe la UN Women muno m’malawi.